Open-access Momwe ophunzira akuyunivesite amachepesela ziphinjo zomwe amakumana nazo pogwila ntchito yosamalira zachilengedwe: Zidziwitso zochokera ku Malawi ndi Zambia

Abstract

Nkhani yofunikira kwambiri yakusintha kwanyengo ikupangisa maiko ambiri kutengapo gawo pantchito zosamalira chilengwedwe. Mwa ena, achinyamata nawo akuonetsa chidwi chochuluka potengapo gawo polimbikisa ntchito zosamalira chilengedwezi. Ngakhale izi zili choncho, achinyamatawa akukumuna ndi ziphinjo zosiyanasiyana kuti akwanilise maloto awowo. Pogwilitsa ntchito tsanamira za kuunikila zothekela mwa munthu muntchito zosiyanasiyana, kafukufukuyu anaunikila maganizo a achinyamata ochokela musukulu za ukachenjede ziwiri, ina yaku Malawi ndipo ina yaku Zambia kuti timvese bwino ziphinjo zomwe achinyamatawa amakumana nazo musukuluzi akafuna kupititsa patsogolo ntchito zosamalira chilengedwe. Zotsatira zakafukufukuyu zaonetsa kuti ngakhale achinyamata akutenga gawo pa ntchito yosamalira zachilengedwe ndipo akudzipereka kwambiri pantchitoyi, amakumananso ndi mavuto osiyanasiyana monga: kusowa kwa chithandizo chochokera ku utsogoleri wamasukulu awo, kusowa kwa zinthu zogwiritsa ntchito pogwira ntchito imeneyi, zikhulupiriro za anthu a zikhalidwe zosiyanasiyana komanso kupondelezedwa ndi anthu a udindo m'sukulu zaukachenjedezi. Ngakhale pali mavuto amenewa, ophunzirawa amakhazikitsa njira zosiyanasiyana zothetsela mavuto awo monga: kukhazikitsa ubale ndi mabungwe omwe si aboma kuti azipeza thandizo la zida zogwilira ntchito, kugwiritsa bwino ntchito masamba a mchezo pofalitsa ntchito zawo, komanso kukhala nawo mmagulu a anthu olimbikitsa za kasamaliridwe kachilengedwe. Zotsatira za Kafukufukuyu zikutsindikiza nsanamira zosiyanasiyana zomwe zingathandize achinyamata kutengapo gawo posamalira zachilengwedwe ku maiko akummwela kwa Afrika polimbikitsa kupilira komanso kuthekela komwe achinyamata ali nako popititsa patsogolo ntchito zosamalira chilengedwe.

Kugwila ntchito zosamalira chilengedwe; ophunzira; kuthekela; kuchepesa ziphinjo


location_on
Journal of Student Affairs in Africa 7 Walmer Road, Woodstock, Cape Town, Western Cape, ZA, 7925, Tel: +27 83 350 5959 - E-mail: editor@africanminds.co.za
rss_feed Stay informed of issues for this journal through your RSS reader
Go to top